DZIKO LA IRAN LAKHADZIKITSA TSIKU LADZISANKHO ZA MTSOGOLERI WADZIKO WATSOPANO
Kutsatira imfa ya mtsogoleri wa dziko la Iran, Ebrahim Raisi, nyumba youlutsa uthenga yadzikoli yalengedza za kukhadzikitsidwa kwa tsiku lodzachita zisankho zina pofuna kusankha mtsogoleri watsopano wa dzikoli. Nyumba youlutsa uthangayo yalengedza kuti zisankho zidzachitika mwezi wa chinayi ndi chimodzi pa 28 chaka cha 2024.
Imfa
ya Mtsogoleri wa dziko la Iran yachitika la Mulungu sabata lomwelino pa 19 pamene
ndege yomwe adakwera mtsogoleriyu idachita ngozi mmalire a dziko la Iran ndi
Azerbaijani chaku mpoto kwa dzikoli mudera lochedwa Varzagham pa nthawi yomwe
amachokera ku nkumano omwe adali nawo ndi mtsogoleri wa dziko la Azerbaijani,
Ilham Aliyev, kumene amakayendera ntchito yomanga madamu otchedwa Qiz Qalasi
ndi Khodaafarin m’malire a dziko la Iran ndi azerbaijani. Nyumba yofalitsa
mauthenga ya dzikoli lati ngozi ya ndege idachitika la Mulungu mmamawa ndipo
ndegeyo yapezedwa lolemba kumapiri ambali ina ya dzikoli.
Pamalo
angoziwa pafa anthu ena anayi ndi m’modzi kuphatikizapo nduna yoona zamaubale
pakati pamayiko ya dziko la Iran bambo Hossein Ami-Abdollahian.
Kutsatira
ndikukhadzikitsidwa kwa tsiku lodzachita zisankho za mtsogoleri watsopano
mudzikoli, pakadali pano pa mpando wa pulezidenti asankhirapo mtsogoleri wina
woti agwilizire pa mpandowu pamene akudikilira kudzachita zisankho mwezi wa
mmawa pa 28. Bambo Mohammad Mokhber ndiomwe asankhidwa kukhala mtsogoleri wa
dziko pakadali pano, ndipo pa mpando wa unduna owona zamaubale pakati pamayiko
akhadzikitsapo mtsogoleri yemwe adali wachiwiri wa a Hossein Ami-Abdollahian,
ndipo pakadali pano bambo Ali Bagheri Kani ndiomwe asankhidwa kukhala nduna
yaikulu yowona zamaubale pakati pa mayiko mudzikomo.
Lero lachiwiri pa 21 mwezi wa chinayi, mwambo wa maliro a mtsogoleri wa Iran bambo Raisi ndi anthu ena asanu ndi awiri omwe adakhuzidwa ndi ngozi ya ndege wayamba ndipo mwambowu ukuchitikira mu dera lina lochedwa Tabriz lomwe likupedzeka kumadzulo kwa dziko la Iran. Boma la Iran kudzela mu ulamuliro wa nduna yaikulu bambo Ali Khamenei mu dzikoli yalamula kuti dzikoli likhala likuchita mwambo wa malirowu kwa masiku anayi polira maliro a mtsogoleri wadzikoyi kuphatikizapo adzitsogoleri ena onse omwe ataya miyoyo pangozi yachitikayi.
Kanema
wa dzikoli walengedza kuti boma la Iran lipitilira kugwira ntchito zake popanda
chovuta chilichonse ngati mmene zimakhalira nthawi zonse popanda chilichonse chovuta
kapena kusokoneza, ngakhale dzikoli lakumana ndi mavuto aakulu chonchi potaya
mtsogoleri wawo ndi azitsogoleri ena asanu nd awiri pa ngozi ya ndege.
Mayiko
ambiri komanso adzitsogoleri ochuluka ndi okhudzidwa kwambiri ndi imfa ya Bambo
Raisi, adzitsogoleri amayiko angapo apereka mafuno achisoni ku dziko la Iran
komanso ndi anthu onse okhudzika pa imfa ya azitsogoleri amenewa. Nduna yaikulu
ya dziko la Pakistan bambo Shehbaz Sharif yafotokodza kukhudzika kwawo ndi imfa
ya mtsogoleri wa iran ndipo iyo yawafotokoza bambo Raisi ndi bambo
Amir-abdollahhian ngati mnzika zokondedwa mu dziko la Iran.
Nyumba
wofalitsa mauthenga mu dziko la Iran yotchedwa Islamic Republic of Iran
Broadcasting (IRIB) yalengeza kuti pakadali pano chomwe chadzetsa kuti ngozi ya
ndege yomwe adakwera pulezidenti wa dzikoli kuti ichitike sichikudziwika ndipo
padakali pano kafukufuku akuchitika kuti apedze chomwe chidadzetsa ngozi ya
ndegeyi. Izi zili chonchi ngakhale makanema ena amayiko otsiyanatsiyana
akufotokoza kuti ngoziyi yachitika chifukwa cha nyengo yovuta omwe idalipo la
Mulungu kumalo komwe ndegeyi imadutsa, ndipo ena akufotokoza kuti zikhodza
kukhala kut ndegeyi idachitidwa chipongwe ndi anthu ena.


This comment has been removed by the author.
ReplyDeleteSad news
ReplyDeleteZomvesa chisoni kwambili
ReplyDeleteZomvesa chisoni zedi
ReplyDelete