DZIKO LA IRAN LAKHADZIKITSA TSIKU LADZISANKHO ZA MTSOGOLERI WADZIKO WATSOPANO


Kutsatira imfa ya mtsogoleri wa dziko la Iran, Ebrahim Raisi, nyumba youlutsa uthenga yadzikoli yalengedza za kukhadzikitsidwa kwa tsiku lodzachita zisankho zina pofuna kusankha mtsogoleri watsopano wa dzikoli. Nyumba youlutsa uthangayo yalengedza kuti zisankho zidzachitika mwezi wa chinayi ndi chimodzi pa 28 chaka cha 2024.

Imfa ya Mtsogoleri wa dziko la Iran yachitika la Mulungu sabata lomwelino pa 19 pamene ndege yomwe adakwera mtsogoleriyu idachita ngozi mmalire a dziko la Iran ndi Azerbaijani chaku mpoto kwa dzikoli mudera lochedwa Varzagham pa nthawi yomwe amachokera ku nkumano omwe adali nawo ndi mtsogoleri wa dziko la Azerbaijani, Ilham Aliyev, kumene amakayendera ntchito yomanga madamu otchedwa Qiz Qalasi ndi Khodaafarin m’malire a dziko la Iran ndi azerbaijani. Nyumba yofalitsa mauthenga ya dzikoli lati ngozi ya ndege idachitika la Mulungu mmamawa ndipo ndegeyo yapezedwa lolemba kumapiri ambali ina ya dzikoli.

Pamalo angoziwa pafa anthu ena anayi ndi m’modzi kuphatikizapo nduna yoona zamaubale pakati pamayiko ya dziko la Iran bambo Hossein Ami-Abdollahian.

Kutsatira ndikukhadzikitsidwa kwa tsiku lodzachita zisankho za mtsogoleri watsopano mudzikoli, pakadali pano pa mpando wa pulezidenti asankhirapo mtsogoleri wina woti agwilizire pa mpandowu pamene akudikilira kudzachita zisankho mwezi wa mmawa pa 28. Bambo Mohammad Mokhber ndiomwe asankhidwa kukhala mtsogoleri wa dziko pakadali pano, ndipo pa mpando wa unduna owona zamaubale pakati pamayiko akhadzikitsapo mtsogoleri yemwe adali wachiwiri wa a Hossein Ami-Abdollahian, ndipo pakadali pano bambo Ali Bagheri Kani ndiomwe asankhidwa kukhala nduna yaikulu yowona zamaubale pakati pa mayiko mudzikomo.

Lero lachiwiri pa 21 mwezi wa chinayi, mwambo wa maliro a mtsogoleri wa Iran bambo Raisi ndi anthu ena asanu ndi awiri omwe adakhuzidwa ndi ngozi ya ndege wayamba ndipo mwambowu ukuchitikira mu dera lina lochedwa Tabriz lomwe likupedzeka kumadzulo kwa dziko la Iran. Boma la Iran kudzela mu ulamuliro wa nduna yaikulu bambo Ali Khamenei mu dzikoli yalamula kuti dzikoli likhala likuchita mwambo wa malirowu kwa masiku anayi polira maliro a mtsogoleri wadzikoyi kuphatikizapo adzitsogoleri ena onse omwe ataya miyoyo pangozi yachitikayi.


Ngozi imeneyi yachitika mu nthawi imene dziko la Iran likudutsa munyengo zovuta  maka kunkhani zokhuza khondo yomwe ikuchitika pakati pa dziko la Ukraine ndi dziko la Russia. Dziko la Iran lakhala likuthandiza dziko la Russia kumbali ya zokambirana zosiyanasiyana komanso kumbali yokhudza zankhondo kuchokera nthawi yomwe dziko la Russia lidayamba kuchita nkhondo ndi dziko la Ukraine mu chaka cha 2022 mwezi wachiwiri.

Bambo Raisi adali nd zaka 63 ndipo iwo alamulira dziko la Iran kwa zaka zinayi kuchokera  mu chaka cha 2021 pomwe iwo adatsankhidwa kukhala mtsogoleri wa dziko.

Kanema wa dzikoli walengedza kuti boma la Iran lipitilira kugwira ntchito zake popanda chovuta chilichonse ngati mmene zimakhalira nthawi zonse popanda chilichonse chovuta kapena kusokoneza, ngakhale dzikoli lakumana ndi mavuto aakulu chonchi potaya mtsogoleri wawo ndi azitsogoleri ena asanu nd awiri pa ngozi ya ndege.

Mayiko ambiri komanso adzitsogoleri ochuluka ndi okhudzidwa kwambiri ndi imfa ya Bambo Raisi, adzitsogoleri amayiko angapo apereka mafuno achisoni ku dziko la Iran komanso ndi anthu onse okhudzika pa imfa ya azitsogoleri amenewa. Nduna yaikulu ya dziko la Pakistan bambo Shehbaz Sharif yafotokodza kukhudzika kwawo ndi imfa ya mtsogoleri wa iran ndipo iyo yawafotokoza bambo Raisi ndi bambo Amir-abdollahhian ngati mnzika zokondedwa mu dziko la Iran.

Nyumba wofalitsa mauthenga mu dziko la Iran yotchedwa Islamic Republic of Iran Broadcasting (IRIB) yalengeza kuti pakadali pano chomwe chadzetsa kuti ngozi ya ndege yomwe adakwera pulezidenti wa dzikoli kuti ichitike sichikudziwika ndipo padakali pano kafukufuku akuchitika kuti apedze chomwe chidadzetsa ngozi ya ndegeyi. Izi zili chonchi ngakhale makanema ena amayiko otsiyanatsiyana akufotokoza kuti ngoziyi yachitika chifukwa cha nyengo yovuta omwe idalipo la Mulungu kumalo komwe ndegeyi imadutsa, ndipo ena akufotokoza kuti zikhodza kukhala kut ndegeyi idachitidwa chipongwe ndi anthu ena.

 

Comments

Post a Comment

Popular posts from this blog

MINISTRY OF AGRICULTURE SETS CROP FARM GATE PRICES: MALAWI

MALAWI’S ECONOMY GRINS TO THE IMPACT OF MEGA FARMS

CHAKWERA LAUNCHES AGRICULTURAL MECHANIZATION INITIATIVE