DZIKO LA IRAN LAKHADZIKITSA TSIKU LADZISANKHO ZA MTSOGOLERI WADZIKO WATSOPANO
Kutsatira imfa ya mtsogoleri wa dziko la Iran, Ebrahim Raisi, nyumba youlutsa uthenga yadzikoli yalengedza za kukhadzikitsidwa kwa tsiku lodzachita zisankho zina pofuna kusankha mtsogoleri watsopano wa dzikoli. Nyumba youlutsa uthangayo yalengedza kuti zisankho zidzachitika mwezi wa chinayi ndi chimodzi pa 28 chaka cha 2024. Imfa ya Mtsogoleri wa dziko la Iran yachitika la Mulungu sabata lomwelino pa 19 pamene ndege yomwe adakwera mtsogoleriyu idachita ngozi mmalire a dziko la Iran ndi Azerbaijani chaku mpoto kwa dzikoli mudera lochedwa Varzagham pa nthawi yomwe amachokera ku nkumano omwe adali nawo ndi mtsogoleri wa dziko la Azerbaijani, Ilham Aliyev, kumene amakayendera ntchito yomanga madamu otchedwa Qiz Qalasi ndi Khodaafarin m’malire a dziko la Iran ndi azerbaijani. Nyumba yofalitsa mauthenga ya dzikoli lati ngozi ya ndege idachitika la Mulungu mmamawa ndipo ndegeyo yapezedwa lolemba kumapiri ambali ina ya dzikoli. Pamalo angoziwa pafa anthu ena anayi ndi m’modzi kuphatikizapo...